Luke 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iweyo sudakhulupirire zimene ndanenazi, koma zidzachitika ndithu pa nthaŵi yake. Nchifukwa chake udzakhala duu, osatha kulankhula, kufikira tsiku lodzachitika zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzacitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau, anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yace.