Luke 1:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamtuma kwa namwali wina wosadziŵa mwamuna amene anali atafunsidwa mbeta ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la mfumu Davide. Namwaliyo dzina lake anali Maria.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lace Yosefe, wa pfuko la Davine; ndipo dzina lace la namwaliyo ndilo Mariya.