Luke 1:66 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse amene ankazimva, ankazilingalira m'mitima mwao, ndi kumadzifunsa kuti, “Kodi mwana ameneyu adzakhala munthu wotani?” Pakuti zinkachita kuwonekeratu kuti Ambuye anali naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nangamwana uyu adzakhala wotani? Pakuti 13 dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.