Luke 1:80 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana uja Yohane ankakula nasanduka wa mkhalidwe wamphamvu. Pambuyo pake adakhala ku chipululu mpaka tsiku limene adadziwonetsa poyera pakati pa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wace, ndipo 23 iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israyeli.