Luke 10:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiri awiri pamaso pace ku mudzi uli wonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.