Luke 10:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika m'Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka iwe, Korazini! tsoka iwe Betsaida! cifukwa kuti zikadacitika m'Turo ndi Sidoni zamphamvuzi zidacitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi obvala ciguduli ndi phulusa.