Luke 10:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzicuruka, koma anchito acepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe anchito kukututa kwace.