Luke 10:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira iye.