Luke 10:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anayankha nati, 3 Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.