Luke 10:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Msamariya wina ali pa ulendo wace anadzapali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa cifundo,