Luke 10:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khalani m'nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikirako nkukaloŵa ku nyumba zina ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wanchito ayenera mphotho yace; musacokacoka m'nyumba.