Luke 11:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakukhala iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ace anati kwa iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ace.