Luke 11:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo m'banja akayamba kukangana, banjalo limapasuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m'kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwake igwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m'kati mwace upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwace igwa.