Luke 11:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzani kuti ndinu olakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi Beelzebule, ana anu aziturutsa ndi yani? Mwa ici iwo adzakhala oweruza anu.