Luke 11:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako. Ndipo ukapanda kuŵapeza, umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene pali ponse mzimu wonyansa ukaturuka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinaturukako;