Luke 11:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, mai wina pakati pa anthu ambiri aja adakweza mau namuuza kuti, “Ngwodala mai amene adabalani nkukuyamwitsani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakunena izi iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.