Luke 11:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu ankachulukirachulukira, Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ngoipa, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene gulu la anthu limachuluka, Yesu anati, “Uno ndi mʼbado oyipa. Umafuna kuona chizindikiro chodabwitsa. Koma sadzachiona kupatula chizindikiro chija cha Yona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna cizindikilo, ndipo cizindikilo sicidzapatsidwa kwa uwu koma cizindikilo ca Yona.