Luke 11:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lachiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi anthu a mʼbado uno ndipo idzawatsutsa, chifukwa iyo inachokera kumapeto a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza ku'cokera ku malekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomo; ndipo onani, woposa Solomo ali pano.