Luke 11:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu sati akayatsa nyale, nkuiika m'chipinda chapansi kapena kuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumbamo aone kuŵala kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'cipinda capansi, kapena pansi pa muyeso, koma pa coikapo cace, kuti iwo akulowamo aone kuunika.