Luke 11:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati kuŵala kukhala m'thupi monse, popanda mdima pena paliponse, apo thupi lonse lidzakhala loŵala, monga pamene nyale ikukuunikira ndi kuŵala kwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lace lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwace ikuunikira iwe.