Luke 11:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, cha timbeu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbeu zakudimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsoka inu, Afarisi! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa cakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka ciweruziro ndi cikondi ca Mulungu; mwenzi mutacita izi, ndi kusasiya zinazo.