Luke 11:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Muli ndi tsokanso, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wosautsa kunyamula, pamene inuyo simumkhudzako mpang'ono pomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anayankha kuti, “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Tsoka inunso, acilamulo inul cifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi cala canu cimodzi.