Luke 11:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mukutsimikiza kuti mukuvomereza ntchito za makolo anuwo, popeza kuti iwowo adapha aneneriwo, inuyo nkumamanga ziliza zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco muli mboni, ndipo mubvomera nchito za makolo anu; cifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.