Luke 11:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati, ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa icinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;