Luke 11:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuyambira kuphedwa kwa Abele, mpaka kuphedwa kwa Zakariya amene adaphedwera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuyambira mwazi wa 1 Abele kufikira mwazi wa 2 Zakariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kacisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.