Luke 11:52 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muli ndi tsoka, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mudalanda kiyi yotsekulira anthu nzeru. Inu nomwe sumudaloŵe, ndipo mudatsekereza amene ankafuna kuloŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mwachotsa kiyi wachidziwitso inu eni akenu musanalowemo, ndipo mwatsekerezanso iwo amene amalowa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
3 Tsoka inu, acilamulo! cifukwa munacotsa cifungulo ca nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.