Luke 12:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti chikhamu cha anthu zikwi ndi zikwi chikusonkhana, kotero kuti anthuwo ankangopondana. Yesu adayamba kulankhula ndi ophunzira ake poyamba, Adati, “Chenjerani ndi chofufumitsira buledi cha Afarisi, chimene chili chiphamaso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo, anthu miyandamiyanda atasonkhana, ndi kumapondanapondana, Yesu anayamba kuyankhula poyamba kwa ophunzira ake, nati, “Chenjereni ndi yisiti wa Afarisi, amene ndi chinyengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo pamene anthu a zikwi zikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, iye anayamba kunena kwa ophunzira ace poyamba, Tacenierani nokha ndi cotupitsa mikate ca Afarisi, cimeneciri cinyengo.