Luke 12:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Akadzakutengerani ku milandu ku nyumba zamapemphero, kapena kwa mafumu ndiponso kwa akulu a Boma, musati mudzavutike nkumati, ‘Kaya ndikayankha bwanji? Ndikanena chiyani?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene pali ponse adzamuka nanu ku mlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena ciani;