Luke 12:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani maluŵa m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomoni, mu ulemerero wake wonse sanavale ngati limodzi la awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa nchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemerero wace wonse, sanabvala ngati limodzi la awa.