Luke 12:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wa kuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati Mulungu abveka kotere maudzu a kuthengo akukhala lero, ndipo mawa aponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?