Luke 12:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngodala antchito amene mbuye wao pofika, aŵapeza ali maso. Ndithu ndikunenetsa kuti adzadzikonzekera, nadzaŵakhazika podyera, ndipo adzabwera nkumaŵatumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'cuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.