Luke 12:53 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mai adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mai wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wa mwana wao, ndipo mkaziyo adzakangana ndi apongozi akewo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzatsutsana atate ndi mwana wace, ndi mwana ndi atate wace; amace adzatsutsana ndi mwana wamkazi'l ndi mwana wamkazi ndi amace, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wace, ndi mkaziyo ndi mpongozi wace.