Luke 12:56 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu anthu achiphamaso, mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi a kuthambo, koma bwanji simutha kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika masiku omwe ano?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo yino?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yace ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengoyino?