Luke 12:58 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga pamene ukupita ndi mnzako wamlandu kwa woweruza, uyesetse kukonza mlanduwo mukali pa njira, kuwopa kuti angakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m'nyumba yandende.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mukupita kwa woweruza ndi amene munalakwirana naye, yesetsani kwambiri kuti muyanjane naye mʼnjiramo, chifukwa mukapanda kutero akhoza kukutengerani ku bwalo la milandu ndipo woweruzayo adzakuperekani kwa woyangʼanira ndende, ndipo woyangʼanira ndendeyo adzakuponyani mʼndende.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti 8 pamene ulikupita naye mnzako wa miandu kwa woweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa woweruza, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, ndi msilikari angaponye iwe m'nyumba yandende.