Luke 13:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena amene anali pomwepo adadza kwa Yesu, nayamba kumsimbira za Agalileya amene Pilato adaalamula kuti aphedwe, pamene iwo ankapereka nsembe zao kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasanganiza mwazi wao ndi nsembe zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo panali ena amene analipo omwe amamuwuza Yesu za Agalileya amene magazi awo Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza iye za Agalileya, amene Pilato anasanganiza mwazi wao ndi nsembe zao.