Luke 13:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake. Idamera nisanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wace wace, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zace.