Luke 13:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uli ngati yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza ndi ufa wambiri mpaka anafufumitsa ufawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ufanana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazianatenga, nacibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupa wonsewo,