Luke 13:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwini nyumba adzanyamuka nkutseka pa khomo. Pamenepo, okhala panjanu mudzayamba kugogoda nkumanena kuti, ‘Ambuye, titsekulireni.’ Koma Iye adzakuyankhani kuti, ‘Sindikudziŵa kumene mukuchokera.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’ “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pacitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene mucokerako;