Luke 13:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Iye adzakuuzani kuti, ‘Pepani, sindikudziŵa kumene mukuchokera. Chokani apa nonsenu, anthu ochita zoipa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene mucokera inu; cokani pa Ine, nonse akucita cosalungama,