Luke 13:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Pitani kaiwuzeni nkhandweyo kuti ndikutulutsa mizimu yoipa ndiponso ndikuchiritsa anthu lero ndi maŵa, ndipo mkucha mpamene nditsirize ntchito yanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditurutsa ziwanda, nditsiriza maciritso lero ndi mawa, ndipo mkuca nditsirizidwa.