Luke 13:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m'mapiko ake, ndipo simunafunai!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! ha! kawiri kawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ace m'mapiko ace, ndipo simunafunai!