Luke 13:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga anthu aja 18 amene nyumba yosanja idaŵagwera ku Siloamu nkuŵapha? Kodi mukuyesa kuti iwowo anali ophwanya malamulo koposa anthu ena onse okhala m'Yerusalemu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m'Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kapena anthu 18 aja amene anafa nsanja ya Siloamu itawagwera, kodi mukuganiza kuti iwo aja anali ochimwa kwambiri kuposa onse amene amakhala mu Yerusalemu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m'Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?