Luke 13:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaŵaphera fanizo, adati, “Munthu wina anali ndi mkuyu wobzalidwa m'munda wake wamphesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wamphesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Iye anawawuza fanizo kuti, “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu, umene anadzala mʼmunda wamphesa, ndipo Iye anapita kukayangʼana zipatso, koma sanazipeze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wookam'munda wace wamphesa. Ndipo anadza nafuna cipatso pa uwu, koma anapeza palibe.