Luke 14:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza cakudya ca pausana kapena ca madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a pfuko lako, kapena anansi ako eni cuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.