Luke 14:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wantchitoyo atabwerako adadzasimbira mbuye wake zonsezo. Apo mwini nyumbayo adapsa mtima, nauza wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msanga ku miseu yaikulu ndi yaing'ono ya mumzinda muno ukapeze anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi opunduka, ukabwere nawo kuno.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mudzi, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wace zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wace, Turuka msanga, pita kumakwalala ndi ku njira za mudzi, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.