Luke 14:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wace ndi amace, ndi mkazi wace, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ace, inde ndi moyo wace womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.