Luke 14:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzace, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akuru ngati akhoza ndi asilikari ace zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikari zikwi makumi awiri?