Luke 14:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adaŵafunsa kuti, “Ndani mwa inu, bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime pa tsiku la Sabata, sangaitulutse pa Sabata pomwepo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Iye anawafunsa kuti, “Kodi ngati mmodzi mwa inu ali ndi mwana wamwamuna kapena ngʼombe imene yagwera mʼchitsime tsiku la Sabata, kodi simungamuvuwulemo tsiku lomwelo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu buru wace kapena ng'ombe yace itagwa m'citsime, ndipo sadzaiturutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?