Luke 15:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala cimwemwe Kumwamba cifukwa ca wocimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.