Luke 16:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene anali ndi kapitao wake. Anthu adaadzamneneza kapitaoyo kuti akumwaza chuma cha mbuye wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye ananenanso kwa ophunzira ace, Panali munthu mwini cuma, anali ndi kapitao wace; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza cuma cace.